Saturday, May 28, 2011

Masewero a Ragibe apita patsogolo kuThyolo

WOLEMBA RICHARD CHIROMBO
Boma laThyolo lalimbikitsa Masewero aRagibe (Rugby) pakati paanyamata
ndiatsikana am’sukulu zasekondale ngati mbali imodzi yoonetsetsa kuti
dziko laMalawi likhalenso nditimu yafuko yamphavu pamasewerawa.
Masewero aRagibe, omwe ndiotchuka kwambiri m’maiko monga South Africa
ndiNamibia, adalowa pansi m’dziko laMalawi, ngakhale kuti azungu ena
achitsamunda amkachita masewerowa kuyambira zaka zam’ma1943.
Masewerowa adatchuka kwambiri m’dziko muno m’ma1970, pomwe patimu omwe
amapezeka kuZomba, Thyolo komanso Blantyre (paBlantyre Sports Club).
Dziko laMalawi lidali ndiosewera monga Costas Scordis, omwe
adathandiza kuti matimu am’dziko muno azichita bwino akakumana
ndimatimu monga Zambia ndiNamibia.
Koma, pazifukwa zosadziwika bwinobwino, masewerowa aangoferatu m’dziko
muno. Nkhani yosangalatsa ndiyokuti akuluakulu aBungwe laRugby
Association of Malawi (RAM), lomwe pakadali pano akufuna kulilembetsa
kuMalawi National Council of Sports (MNCS).
A Serj Mwatiha, omwe akugwirizira udindo wawapampando waRAM, adauza
mtolankhani wathu loweluka lapitali kuti boma laThyolo latsogola
kwambiri pamasewera aRagibe.
“Masewerawa apita patsogolo kwambiri kuThyolo, ndipo akuseweredwa
ndiana ambiri m’sukulu monga Luchenza ndiMendulo Community Day
Secondary (CDSS). Nalo boma laMulanje silikutsalira m’mbuyo, ndipo
Rabibe ikuseweredwa papulaimale yaLomola,” adatero aMwatiha.
AMwatiha, omwe ndimphunzitsi wapaLuchenza CDSS, adati izi zili
chomwecho chifukwa chakhama lamzika ina yakuScortland, aCharles
Fewcett, omwe adayambitsa masewerowa m’sukulu ataona kuti ana ambiri
amatenga kachilombo koyambitsa matenda aEdzi, kaHIV, kamba kosowa
chochita.

Rugby at Blantyre Sports Club

Loweluka lapitali, matimu ochokera kuKasungu (Kamuzu Academy), Thyolo,
Blantyre (Saint Andrews International High Schoo ndiKalibu Academy)
adakumana pabwalo lazamasewera laBlantyre Sports Club ndicholinga
chofuna kupatsa akuluakulu oyendetsa Ragibe mwayi osankha osewera omwe
adzamenye mutimu yaMalawi akadzaikhazikitsanso.
Pakadali pano, bungwe laRAM lili pakalikiliki ofuna kulembetsa
ndiMNCS. RAM idauzidwa kuti idzalembetsedwa ikadzakwanitsa kukhala
ndimatimu 10 aRagibe m’dziko muno, koma zikalata zones zoyenera
kulembetsera timu adamaliza kale kukonza, malingana ndiaMwatiha.

No comments: