Saturday, May 28, 2011

Masewero akiriketi akubwerera m’chimake’

Wolemba Richard Chirombo

Malawi National Cricket Team players training at St. Andrews International High School in Blantyre

Akuluakulu omwe akugwirizira ntchito yoyendetsa bungwe yoyang’anira
masewero akiriketi m’dziko muno, laMalawi Cricket Union (MCU), ati
ntchito yokonzanso zinthu zomwe zimkalakwika ikuyenda bwino.
Wapampando waMCU, a Dave Thompson, adauza mtolankhani wathu kuti,
mwazina, bungweli lapanga kale ndondomeko yotukulira masewero
akiriketi m’dziko muno, laika ndondomeko zokhwima zoyendetsera chuma,
komanso latsala pang’ono kumaliza ntchito yopanga tsamba lofotokoza
zamasewerowa kuMalawi pamakina akompyuta a intaneti, motsatira zomwe
akuluakulu amasewerowa muAfrica ndipadziko lapansi adalangizira
kumayambiriro achaka chino.
Izi zikutsatira kuphwasula kwakomiti yomwe imkayendetsa masewerowa
m’dziko kumayambiriro kwachaka chino, mabungwe oyendetsa masewero
akiriketi padziko lonse lapansi aInternational Cricket Council (ICC)
komanso bungwe lomwe limayang’anira kiriketi muAfrica laAfrica Cricket
Association (ACA) atasonyeza kusakhutitsidwa ndimomwe zimayendera
zinthu kuMCU.
Malingana ndilipoti loyembekezera lowunika zakayendetsedwe kachuma
kuMCU, lomwe adakonza ndi oyendetsa ntchito zothandiza komanso
kuonetsetsa kuti mamembala aICC akuAfrica akutsatira ndondomeko
zoyenera zoyendetsera kiriketi aGoodlove Poswa mothandizana ndiaGraham
McMillan- omwe amalumikiza ntchito zotukula kiriket kuAfrica- zinthu
zambiri sizimayenda bwino m’dziko muno.
Mwazina, akuluakuluwa adati zikalata zokhudzana ndikayendetsedwe
kachuma sizimasungidwa, padalibe yemwe amalemba zochitika pamisonkhano
yaakuluakulu abungweli, anthu amangogwira ntchito popanda m’gwirizano
uliwonse ndiowalemba ntchito (MCU), panalibe ndondomeko yofotokoza
zakasamalidwe kakatundu wabungweli, komanso malipoti azachuma omwe
amaperekedwa kuICC amkasiyana ndimalisiti omwe adali m’mabuku abungwe
laMCU kuno kumudzi.
Zonsezi zidapangitsa kuti komiti yoyendetsa masewerowa kuno kumudzi
ayithetse m’mwezi waFeburuwale chaka chino, ndikukhazikitsa komiti
yongogwirizira yomwe imalize ntchito yake kumayambiriro kwamwezi
waOkotobala chaka chino.
Polankhulapo pazamomwe ikuyendera ntchito yoonetsetsa kuti masewerowa
abwerera m’chimake m’dziko muno, aThompson adati zambiri zomwe
adalangiza mabungwe aICC ndiACA zayamba kutsatidwa, chinthu chomwe
chapangitsa kuti anthu akhalenso ndichidwi ndmasewerowa.
“Zinthu zikuyenda bwino chifukwa tili ndianthu odzipereka kuyendetsa
ntchitoyi. Nayonso timu yakiriketi yadziko lino yayamba kumenya
ndimayiko ena, chinthu chomwe chikutilimbikitsa ndikutipatsa
chikhulupiriro kuti, pofika mwezi waOkotobala, tikhala titakwaniritsa
zonse zomwe tidalangizidwa,” adatero aThompson.
Mwazina, komiti yogwirizirayi- yomwe ili ndiakuluakulu ena monga Robin
Tiffin-Roberts, Bhavesh Dhanesha, Jayendra Khe,ndiVivek Ganesan-
yathandiza kuti timu yaMalawi ikachite nawo masewero amaiko omwe
alimugawo lachiwiri lakiriketi muAfrica, la ICC/ACA Division 2 T20
Tournament, omwe adayamba pa14 Meyi sabata latha ndipo adatha pa
19Meyi kuBenoni m’dziko laSouth Africa.
Dziko laMalawi lidali mugulu loyamba (Pool A), ndipo lidatumiza
osewera khumi ndimphambu zinayi, komanso owayang’anira awiri.
Dziko lino lidakwezedwa kufika mugawo lachiwiri (Division 2)
litachinya matimu onse amuAfrica pampikisano wagawo lachitatu
(Division 3) omwe udachitikira m’dziko muno m’chaka cha2009.

No comments: