WOLEMBA RICHARD CHIROMBO
Bungwe laPeople’s Federation for National Peace and Development
(Pefenap), lomwe limalimbikitsa zabata ndimtendere, layamikira unduna
woyang’anira zachitetezo chaanthu polimbikitsa ntchito zothana
ndiumbanda wamfuti, chinthu chomwe akuti chingapangitse kuti madera
akumidzi atukuke mwachangu.
Mkulu wabungweli, aEdward Chaka, adati kafukufuku yemwe bungwe lawo
lidachita miyezi isanu yapitayi waonetsa kuti m’chitidwe okuba
moopseza ndimfuti wachepa nditheka, chinthu chomwe adati chilimbikitsa
anthu omwe alindintchito zamalonda m’matauni kuganiza zopita kumidzi
popeza chitetezo Chayamba kukhwima m’madera onse.
“M’chitidwe okuba ndimfuti umabwezeretsa chitukuko m’mbuyo. Ngakhale
anthu ena amalonda akudandaula kuti umbanda wamfuti ukuopseza
chitetezo, makamaka chaAmalawi achimwenye, kafukufuku wathu waonetsa
kuti zinthu ziliko bwino kusiyana ndimomwe zidalili zaka zinayi
zapitazo,” adatero aChaka.
Mkuluyu adawonjezera kuti anthu ngakhale amwenye ambiri omwe
adafunsidwa zamaganizo awo adasonjeza kukhutira ndichitetezo, ngakhale
ambiri ayiwo adapempha kuti ogwira ntchito zachitetezo
asamangokhwimitsa chitetezo masana okha, popeza ntchito zambiri
zaumbanda zimachitikanso usiku.
No comments:
Post a Comment