WOLEMBA RICHARD CHIROMBO
Mgwirizano wamabungwe olimbikitsa ntchito zaumoyo m’dziko muno,
laMalawi Heath Equity Network (MHEN), lapempha boma kuti libwezeretse
zinthu zina zomwe zimalimbikitsa ntchito zaumoyo ngati likufuna kuti
mzika zake zipitilire kukhala zathanzi.
Oyang’anira ntchito zaMHEN m’dziko muno, aMartha Kwataine, adati,
mwazina, kuchotsa kwandalama zomwe unduna wazaumoyo umapereka kwaana
omwe amaphunzira zaunamwino ndiudotolo m’sukulu zam’dziko muno
kungapangitse kuti ntchito zaumoyo zibwerere pansi.
“M’mene zilili panopa, ana ambiri sazikwanitsa kupeza ndalama
zolipilira maphunziro aunamwino ndiudotolo, chinthu chomwe chipangitse
kuti anthu ogwira ntchito zamtunduwu achepe,” adatero aKwataine.
Iwo adati zimenezi zionjezeranso pamavuto omwe alipo kale m’dziko
muno, ndipo adatchulapo zazinthu monga kusowa kwandalama zokonzera
zipatala, kuchepa kwaanthu ogwira ntchitozi, komanso kutaya anthu
aluso lawo omwe akumakhamukira kuzipatala zakunja kukagwira ntchito
zamalipiro apamwamba.
Panthawi yomwe unduna wazaumoyo udalengeza kuti wasiya kuonjezera
kangachepe kundalama zomwe anthu opanga zaunamwino ndiudotolo ama
No comments:
Post a Comment