Friday, July 15, 2011

UTHENGA KWA A MALAWI ONSE-PAMOMWE DZIKO LATHU LIKUYENDERA NDIZOFUNIKA KUSINTHA.

UTHENGA KWA A MALAWI ONSE-PAMOMWE DZIKO LATHU LIKUYENDERA NDIZOFUNIKA KUSINTHA.

Malawi Watsopani Ngotheka!

Inu nonse a Malawi mukudziwa kuti mu zaka zisanu zoyamba za ulamuliro wa pulezidenti Bingu wa Mutharika anthu tinatangwanika ndikuona ngati tiona zeni zeni ngati dziko. Ife ngati anthu amene timatsatira mwandondomeko zakayendetsedwe ka boma la dimokilase komanso potsatira zimene inu a Malawi eni munasankha m’mene tinkasintha kuchoka ku ulamuliro wa chipani chimodzi mzaka za 1992 mpakana 1994.
Malawi tsopano wabwerera mbuyo ndipo wasanduka choseketsa cha anthu zifukwa za zinthu izi:
1. Kusowa ndalama za kunja zomwe timatha kugulira zinthu monga mankhwala, mafuta ndi zina zofunika.
2. Kupereka bizinesi kwa anthu omwe ali pa ubale ndi pulezidenti ndi amtundu wake.
3. Kusamvera malangizo ngakhale ochokera kwa atsogoleri a mipingo ndi zipembedzo.
4. Kudzichemerera ndikusamvera kwake kwa mtsogoleri wadziko lino
5. Kufuna kusandutsa u pulezidenti ngati ufumu pofuna kusiira mng’ono wake mpando wa pulezidenti mopanda kutsatira ndondomeko zoyenera za dimokalase ndi ulamuliro wabwino.
6. Kuchitira nkhanza ndi kusawalemekeza a Malawi ena omwe agwira ntchito yokonza dziko la Malawi mbuyomu komanso ngakhale omwe iye wagwira nawo ntchito chifukwa chomulangiza.
7. Kuthamangitsa anthu othandiza dziko lino komanso otigula malonda athu ngati fodya.
8. Kuopyedza ufulu wachibadwidwe wa a Malawi poopsyeza atsogoleri a mabungwe omwe si a boma komanso manyuzipepala ndi mawailesi omwe si a boma.
9. Posintha malamulo mosaganizira zomwe a Malawi anawakhazikira
10. Kusowa kwa mafuta a galimoto ndi zina zotero kwa nthawi yayitali.
11. Kuletsa kugula mafuta m’zigubu ngakhale galimoto litakuthera mafutawo panjira kapena kunyumba kwanu.
12. Kunyozera zigamulo za ma khoti komanso kuopyeza ogwira ntchito m’makhotimo ndikuwamana malipilo awo motsutsana ndi malamulo.
13. Kukondera popatsa maudindo a boma ndi mabungwe a boma komanso bizinesi kwa anthu a mtundu wake wokha.
14. Kuzunza atsogoleri akale ndi ena monga a pulezidenti opuma powakaniza kupita kuchipatala komanso a Cassim Chilumpha.
15. Kuzunza wachiwiri wa pulezidenti wa dziko a Joyce Banda powachepetsera ndalama za mu ofesi yawo mu bajeti ya chaka chino
16. Kuzikundikira chuma pogula ndi kumanga nyumba 15 kunja ndi kuno komwe pogwiritsa ntchito ndalama zomwe zikanatukula dziko lino.
17. Kupatsa mkaza wake malipiro (salary) pogwira ntchito yothandiza yomwe ena amagwira wosalipidwa.
18. Kumangiridwa nyumba ndi zina ndi kontalakitala (contractor) yemwe akupatsidwa ma kontilakiti a boma mosatsatira ndondomeko.
19. Kusamutsa sukulu ya ukachenjede (University) yoti imangidwe ku Lilongwe kupititsa ku mudzi ndi munda wake ku Ndata ngati ndi yake
20. Kumpatsa galimoto zomwe ziyenera kuyenda ndi anthu ngati pulezidenti ndi wachiwiri wake (convoy) kwa Peter Mutharika atalanda kwa Veep ndi a pulezidenti opuma pamene mchimwene wakeyo ali nduna wamba.
21. Kupereka chimanga mwaulere ku Zimbabwe mopanda chilolezo chochokera kunyumba ya malamulo.
22. Kunamiza a Malawi kuti iye ndiwa nzeru pamene akulephera kuyendetsa dziko.
23. Kutseka sukulu zaukachenjede pamene analumbira kuti muulamuliro wake sukulu zimenezi sizizatsekedwanso.
24. Kunyoza mavenda ndi anthu amalonda.
25. Kuononga ndalama za boma pomanga damu (doko) ku Nsanje popanda kuwafunsa a ku Mozambique omwe akukhudzidwa ndi mbali ina yantchitoyi.
26. Kuwabera anthu omwe akupereka zinthu m’boma ponama ndi nkhani ya funding.
27. Kukhometsa misonkho mosaona kuvutika kwa anthu.
28. Kuopseza atsogoleri a zipani zotsutsa ndi amabungwe amene si a boma
29. Kugwiritsa ndi kuphangira nyumba zoulutsila mau za MBC potukwana amalawi.

Nkhani zonsezi ndi zina zotero zikuonetsa kuti a Pulezidenti athu boma lawakanika kuyendetsa- akuyesa kuti utsogoleri ndi njira yongolemelera ndikutchukirapo. Tsopano nthawi yakwana kuti a Malawi tonse tidzuke ndikuwonetsa kuti mphamvu zoyika ndi kuchotsa munthu pa mpando wa upulezidenti zili ndi ife. Tiyeni tonse pa 20 July tidzatuluke ndi kuyenda pa nseu mwa bata ndi mtendere pakuonetsa kusakondwa ndi m’mene zinthu zili m’dziko muno ndiponso kusakondwera ndi utsogoleri wa a Bingu wa Mutharika.
Ife a Malawi okhudzidwa

No comments: