Friday, July 15, 2011

Uthenga kwa a Malawi: Malawi Wabwino Ndiwotheka

Uthenga kwa a Malawi
“Malawi Wabwino Ndiwotheka”
Tafuna tikudziwitseni a Malawi nonse ndi onse okhudzidwa kuti ife ngati nzika zokhudzidwa takonza zionetsero za padera zomwe zidzachitike mwa mtendere pa 20th July 2011 mu zigawo zonse zitatu za dziko lino.
Zionetsero zimezi zakonzedwa motsatira ufulu omwe tili nawo movomerezeka ndi malamulo a dziko lino kuti tidzawonetse kusakondwa ndi m'mene chuma chikuyendera komanso kulira kwa a Malawi pa nkhani ya demokilase. Cholinga cha zonsezi ndikufuna kuthetsa mchitidwe woyika fundo zachabechabe za chuma komanso ulamulirowosakomera anthu ambiri.
Zionetsero zimenezi zikhala zoyamba zomwe zidzatsatiridwe ndi zionetsero zomwe zidzachitike madera onse a dziko lino pa 17th August 2011.
Mutu wa zionetsero zimenezi ndi "Mgwirizano pakulimbana mwa mtendere ndi fundo zoipa za chuma ndi kayendetsedwe ka dziko kosakomera anthu. Malawi wabwino ndiwotheka"
Zionetsero zidzayenda motere:
Chigawo cha kum'mwera (Blantyre)
M'dipiti udzayambira pa Blantyre District Office kudutsa mu Kamuzu Highway mpaka pa Kamuzu Stadium to ndikukathera ku ma ofesi a city council a Civic Offices

Tikuwapempha a Malawi onse okhala ma dera a Ndirande, Chilomoni, Chilobwe, Bangwe, Zingwangwa, Machinjiri, Mbayani, Chileka, Ludzu ndi onse ozungulira Blantyre ndi maboma ena kuti adzafike ndikuyenda nawo pa tsikuli

Chigawo cha pakati (Lilongwe)
Kuyenda kudzayambira pa galaundi la Community kudutsa ku Old Town ndikukalowa Lilongwe/Kasungu Highway ndikukatsirizira ku City Centre.

Tikupempha a Malawi okhala ma dera a Area 25, Kawale, Biwi, Mchesi, Chitsapo, Area 23, 33, 49, 39, Bunda, Likuni,Mugona ndi onse ozungulira Lilongwe ndi maboma ena m'chigawo cha pakati kuti adzafike ndi kuchita nawo zionetserozi pa tsikuli

Chigawo cha pakati (Mzuzu)

Ulendo udzayambira pa Katoto Ground kudutsa mtauni ndikukathera ku ma ofesi a Mzuzu City Council.

Tikupempha anthu okhala ma dera a Zolo Zolo, Katawa, Chiwanja, Mzilawayingwe, Chasefu ndi ma dera onse azungulira mzinda wa Mzuzu ndi ma boma ena kuti adzafike pa 20th July kudzachita nawo zionetserozi.

Tikupempha a Malawi onse kuti pa tsikuli tiyeni tidzavale chovala chafiyira kuli konse kumene tili ngakhale tilibe mwayi wodzayenda nawo pa zifukwa zosiyanasiyana.

Ngati simungakhale nawo pa zionetserozi chifukwa ndinu wamkulu wa kampani, mwini wake wa kampani, kapena ndinu a polisi, msilikali wa nkhondo kapena ogwira ntchito za boma, chonde tumizani a ntchito a m'nyumba mwanu kuti adzakhale nawo pa mwambo wapaderawu.

Pempho: Zionetsero za tsikuli ndi za mtendere ndipo tikupempha a Malawi onse kuti adzasunge ulemu pa nthawi yomwe tidzakhala tikuyenda. Tiyeni tonse tionetse kwa atsogoleri adziko lino kuti ngakhale akutipondereza, ndife anthu a mtendere komanso ofuna kumanga dziko.

Uwu ndi mwayi wathu tonse kuti tibweretse kusintha powonetsetsa kuti mau athu amveka ndiponso agwiritsidwa ntchito potenga nawo gawo pa zochitika za pa 20th July.

Bwerani nonse tidzayendere limodzi

Patsogolo ndi ufulu wa demokilase! Patsogolo ndi kumenyera ufulu!

No comments: