Anthu omwe adakhudzidwa ndivuto lamphepo yamkuntho m’boma laSalima adadandaula kuti anthu ndimabungwe ambiri akuyika chidwi chawo chonse pangozi yazivomerezi zomwe zidakhudza anthu oposa 4,000 m’boma laKaronga, kuyiwala kuti nawonso akuvutika chifukwa chimphepo yamphavu yomwe idasasula nyumba ndikugwetsa mitengo mwezi watha.
Anthu okhala kuChitala m’boma laSalima adakhudzidwa ndivuto lamphepo yamkuntho paDisembala 19, chaka chatha, chinthu chomwe chidapangitsa kuti nyumba komanso mitengo yamalambe, mtenthanyerere ndiina igwe ndikutchinga njira.
Anthu omwe nyumba zawo zidagwa akusowa mtengo wogwira ndipo akugona muzisakasa.
Zimenezi zidadziwika pomwe bungwe laCentre for Sustainable Development and Alternative Rights (SUDAR) lidakayendera madera omwe akhudzidwa kwambiri ndivutoli litalandira pempho kuchokera kubungwe lina lakuNetherlands, lomwe lidapempha bungweli kuti likawunikew zamavuto omwe adza kamba kamphepoyo.
Malingana ndiaMichael Mtambalika, mkulu wabungweli, bungwe lakunjalo lidapempha SUDAR litamva zavutoli.
“Vutoli litagwa, ife tidafotokozera bungwe lotchedwa Universal Justice lakuNetherlands, ndipo bungweli layamba kale kusonkhetsa thandizo m’dzikolo. Tapeza kuti anthu ambiri akuvutika ndivutoli kuSalima, ena mwaiwo alibe ndichakudya chomwe,” adatero aMtambalika.
Anthu oposa 250 akufunika thandizo lamsanga kuChitala, Malingana ndimafumu ena akuChitala.
M’modzi mwaanthu omwe akhudzidwa ndivutoli, a Linda Kuzimva, adadandaula kuti anthu ambiri ayika chidwi chawo pangozi yakuKaronga, chonsecho kuSalima kunalinso vuto lina lalikulu.
“Tikupempha kuti anthu atikumbuke nafenso popeza tili pamavuto adzaoneni. Tikusowa zakudya monga Likuni phala ndizina,” adatero aKuzimva.
Malingana ndibwanankubwa waboma laSalima, a Gift Lapozo, zinthu monga mapepala apulasitiki komanso zakudya ndizomwe zimafunika m’bomalo.
No comments:
Post a Comment