Khonsolo yamzinda waBlantyre yapereka ndalama zokwana K900, 000 kwamabungwe omwe akugwira ntchito zolimbana ndimatenda aEDZI m’madera osiyanasiyana mukhonsoloyi.
Mkulu wakhonsoloyi aLeycester Bandawe adati akuyembekezera kuti miyoyo yaanthu omwe akukhala ndichiyembekezo ndikachilombo kaHIV, komwe kamayambitsa matenda aEDZI, komanso ana amasiye apindula ndintchito zamabungwe am’midziwa.
ABandawe achenjeza mabungwewa kuti ayenera kugwiritsa ntchito ndalamazi moyenera, ndipo adati mabungwe omwe adzapezeke atasakaza thandizoli adzabweza ndalamazo.
“Ndalama zimenezi ndizaanthu omwe akuvutika m’madera osiyanasiyana chifukwa chosowa thandizo mwina chifukwa chokuti akukhala ndichiyembekezo ndiHIV, kapena ndiana amasiye. Pali mavuto osiyanasiyana omwe anthu oterewa amakumana nawo ndipo akuyembekezera umoyo wabwino kuchokera kwamabungwewa,” adatero aBandawe.
Mabungwe am’madera osiyanasiyana mukhonsolo yaBlantyre akhala akudandaula kuti kuchedwa kwandalama zogwirira ntchito kwapangitsa kuti ntchito zosamalira anthu omwe amadalira thandizo lochokera kubungwe loyendetsa ntchito zokhudzana ndiHIV ndiEDZI laNAC avutike kwambiri.
Ena mwamabungwewa adayambanso manong’onong’o pomanena kuti akuluakulu akhonsolo yaBlantyre adadya ndalama zomwe zimayenera kupita kwaanthu omwe akhudzidwa kwambiri ndimatenda aEDZI, chinthu chomwe chidakhumudwitsa akuluakulu amumzindawu popeza ndalama zidali zisadabwere.
No comments:
Post a Comment