Sunday, December 6, 2009

Anthu okana kusamuka mphepete mwamiseu akulepheretsa ntchito zachitukuko

Akuluakulu amzinda waBlantyre adati akukambiranabe ndianthu okhala m’taunishipi yaMbayani ndimadera ena zaubwino osamuka mphepete mwanjira zomwe akufuna zikhale miseu yaphula, chinthu chomwe chidzapangitse kuti malo ambiri akhale ndimiseu yaphula.
Mbayani ndiimodzi mwamataunishipi amumzinda waBlantyre womwe akhala ndimwayi wokhala ndimseu waphula, koma mkulu wamzinda waBlantyre Dr. Lester Bandawe adadandaula polankhula ndimtolankhani wathu kuti anthu ena sakufuna kusamuka mphepete mwaseu.
A Bandawe adati zimenezi zapangitsa kuti ntchito zachitukuko zichedwe m’madera ambiri, mwinanso kulephereka kumene.
“Chitukuko monga chamiseu yaphula chikamabwera, sipamalephera kukhala nyumba zingapo zoti zigwetsedwe. Chomvetsa chisoni m’chakuti anthu ambiri amavuta zikafika pankhani imeneyi, ndipo izi zikubwezeretsa m’mbuyo ntchito yoika miseu m’boma laBlantyre,” adatero aBandawe.
Iwo adapereka chitsanzo chataunishipi yaMbayani, koma kwaikidwa phula chaka chino patatenga nthawi yaitali anthu akudandaula ndifumbi nthawi yachilimwe komanso matope amnanu nthawi yadzinja. A Bandawe adati pali anthu ena omwe akukanabe kusamuka kuti mseu ukafike kutali.
“Mpaka pano tikukambiranaber ndianthu amenewa,” adatero mkuluyu.
Mzinda waBlantyre udalembera m’gwilizano wamizinda yolemera kwambiri padziko lonse lapansi, omwe umadziwika ndidzina lokuti Cities’ Alliance, ndipo imodzi mwantchito zomwe mzindawu ukufuna kuchita ukalandira thandizo ndikumanga miseu yaphula.
Mzindawu, Malingana ndiaBandawe, ukugwiranso ntchito ndinthambi yamgwirizano wamaiko onse apadziko lapansi pazachitukuko, UNDP, pofuna kuthetsa vuto lakuchuluka kwanyumba yazisakasa mumzindawu.
“Tikufuna kuti chitukuko chifike m’madera onse. Miseu yaphula komanso nyumba zabwino zimapangitsa kuti chitukuko chitsekuke m’madera omwe ndikale onse adalibe danga lotelo,” adatero aBandawe.

No comments: