Woweluza milandu kubwalo laana m’boma laBlantyre, a Esmie Tembenu, adachenjeza Amalawi, makamaka okhala m’madera akumidzi, kuti asamale ndichikho champira wamiyendo chapadziko lonse chomwe chichitikire m’dziko laSouth Africa chaka chamawa.
Polankhula ndimtolankhani wathu sabata latha, aTembenu adati pomwe chikho champirachi chatsala pang’ono kuchitika pakhala anthu ena omwe adzibwera m’dziko muno kufuna kudzatenga ana Achimalawi ponamizira kuti akufuna akawalere bwino, chonsecho akufuna kukawagwiritsa ntchito zadama kuSouth Africa.
“Amalawi ayembekezere kuona anthu ambiri akubwera m’dziko muno kufuna kudzatenga ana, ndipo ndikupempha makamaka anthu am’madera akumidzi kuti asamale ndipo asalole kupereka ana kwaanthu osawadziwa. Pamene chikho champira chapadziko lonse lapansi chatsala pang’ono kuchitika, pakhala zinthu zambiri zomwe zizichitika,” adachenjeza aTembenu.
Iwo adati anthu ena afuna kutengera mwayi kusamveka bwino kwamfundo zina zokhudza katengedwe kaana kuchokera kwamakolo awo kapena owayang’anira kupita m’manja mwaanthu ena. Ina mwamfundozi ndiyokuti mzika zamaiko ena zofuna kutenga ana kuno kumudzi zikhale zoti zakhalapo m’dziko muno kwakanthawi.
Koma mfundoyi sifotokoza mwachindunji zanthawi yeni yeni, zimene adati zingapangitse anthu ena kumatenga ana atangokhala pamalo ogona alendo kwakanthawi kochepa.
Poyankhulapo pankhani yomweyi, woweluza milandu kubwalo lalikulu m’dziko muno, omwenso ndiwapampando wabungwe loona kuti chilungamo chikuchitika kwaana m’dziko muno, a Edward Twea adati mpofunika kuti dziko laMalawi likhazikitse kaundula waana onse omwe angatengedwe ndikuleledwa ndianthu ena kuti pasamachitike chinyengo.
ATwea adatinso mpofunika kuti dziko lino livomereze pangano lokhudza ana otelewa, lomwe adalikhazi kuHague, chinthu chomwe adati chidzathandiza kuti ana am’dziko muno omwe atengedwa ndimzika zamaiko ena adzitetezedwa m’maiko omwe apitawo.
Iwo adati zimenezi zidzathandiza kuti dziko lino lisaluze ana chifukwa chazinthu ngati chikho chapadziko lonse lapansi chomwe chichitike chaka chamawa
No comments:
Post a Comment