Thursday, November 12, 2009

Dziko laGermany lilonjeza kutukula maphunziro kuMalawi

Kazembe wadziko laGermany m’dziko muno, a Rainer Mueller, adati boma
lake ndilokhudzidwa ndikutalika kwamitunda yomwe ophunzira ambiri
am’madera akumidzi amayenda kuti apeze nyumba zophunzirako, ndipo
adalonjeza kuti Dziko lake litenga nawo mbali pantchito yochepetsa
Mavuto amtunduwu.
AMueller, omwe amayankhula lachiwiri pasukulu yapulaimale yaNangungu
m’dera lamfumu yaikulu Makanjira m’boma laMangochi, adati n’zomvetsa
chisoni kuti ana pamene anthu ambiri kumaiko akuUlaya amagwa ulesi
ndinkhani zasukulu, anthu akuAfrica, makamaka dziko laMalawi,
amavutika kwambiri kuti apeze maphunziro abwino.
“Ine ndimakhala okhudzidwa kwambiri ndimavuto omwe ana akuno kuMalawi
amakumana nawo kuti apeze maphunziro abwino, chonsecho ana ambiri
akuUlaya akusiya sukulu masiku ano, ndipo amanena kuti sukulu ilibe
phindu. Boma laGermany lionesetsa kuti lachulukitsa thandizo lomwe
limapereka kunkhani zamaphunziro,” adatero a Mueller.
Iwo adaulula kwaanthu omwe adasonkhana kudzaonerera mwambo opereka
nyumba yophunziriramo kwaana apaNangungu kuti nthawi zina nawonso
amkathawa kusukulu ali mwana poganiza kuti maphunziro alibe phindu,
koma asintha maganizo oterewa ataona m’mene anthu akuAfrica
amakhulupirira maphunziro.
“Tigwira ntchito limodzi ndiboma laMalawi pantchito imeneyi, ndipo
pempho lathu kwaaMalawi ndilokuti adzisamala zinthu zopatsidwa ngati
makalasi ophunziliramo kuti anthu ambiri akhale ndichidwi
chothandiza,” adatero a Mueller.
Bungwe lina loima palokha m’dziko laGermany, lotchedwa Reisende
Werkschule Scholen, lidasankha kumagwira ntchito zomanga makalasi
ophunzilira kuMakanjira, ndipo limapereka buloko yachitatu pasukuluyi.
Bungweli lidamanganso nyumba yamphunzitsi wamkulu ndiyosungiramo
zipangizo zapasukulu.
Mkulu wabungweli, a Michael Von Studnitz, adati bungwe lawo likufuna
kumanga nyumba zophunzirira zambiri m’dziko muno, ndipo adawonjezera
kuti vuto lakuchuluka kwaanthu omwe akusiya sukulu likukula kamba
kosowa nyumba ndizipangizo zabwino zophunzilira.
AStudnitz adati n’cholinga chabungwe lawo kutukula maphunziro m’dziko
muno, chinthu chomwe phungu waderali, lomwe lili kumpoto kwaboma
laMangochi, a Ibrahim Matola adati chithandiza kuchepetsa Mavuto omwe
ana amakumana nawo.
AMatola adati boma lokha silingakwanitse kupanga zinthu zones zomwe
mzika zadziko zimafuna, choncho mabungwe akunja adali ndintchito
yaikulu yoonetsetsa kuti akuthandiza boma.
Phunguyu adagwirizana ndiaMueller pankhani yosamalira katundu
opatsidwa, ndipo adachenjeza kuti mabungwe amakhumudwa ndikusiya
kugwira ntchito m’madera kambakaumbanda ndikusasamala zipangizo.
Reisende Werkschule Scholen idayamba kugwira ntchito kuMangochi
m’chaka cha2001, ndipo lidamangaponso nyumba zophunzirilimo
kuMonkeybay.

No comments: