Thursday, November 12, 2009

Chinamwali chikusokoneza ana sukulu

Pamene boma likulimbikitsa ntchito yothandiza kuti ana ambiri adzipita
kusukulu, akuluakulu ena m’boma laMangochi akupitilizabe kupangitsa
miyambo yachinamwali ana asanatsekele sukulu.
Miyambo yoteleyi akuti ikumapitiliranso ana atatsegulira sukulu,
chinthu chomwe chakwiitsa mkulu oyang’anira maphunziro m’sukulu
zapulaimale m’dera (Zoni yamaphunziro) laMpilipili m’dera lamfumu
yaikulu Makanjira m’bomalo.
Mkuluyu, a Bassanio Kachere, adauza mtolankhani wathu sabata latha
kuti m’chitidwewu wapangitsa kuti nambala yaana omwe akupita kusukulu
ichepe.
Iwo adapereka chitsanzo chasukulu yaNangungu, yomwe adati yakhudzidwa
ndikuchepa kwaana opita kusukulu nthawi imene kuli zinamwali.
“Zinamwali zochitika nthawi yasukulu zikusokoneza maphunziro a ana,
ndipo zikutikhudza kwambiri kuona kuti pali anthu ena omwe akupangabe
zinamwali nthawi yasukulu. Tikupempha makolo kuti awonetsetse kuti
sakutumiza ana awo kuchinamwali nthawi yasukulu,” adatero aKachere.
AKachere adatinso china chomwe chikulepheretsa ana kupita kusukulu
ndim’chitidwe wamakolo ena otumiza ana kuthengo kokaweta mbuzi m’malo
moti anawo apite kusukulu.
“Amenewa ndimavuto aakulu. Komabe tikhoza kuwathetsa pogwira limodzi
ntchito ndianankungwi poonetsetsa kuti zinamwali zisamachitike nthawi
yasukulu,” adatero aKachere.
M’madera ambiri m’dziko muno, miyambo ngati chinamwali ikumachitika
ana akakhala patchuthi chasukulu, ndipo ikumatha anawo asanatsegulire
mlingo ophunzilira wina. Kusunga chikhalidwe ndimsanamira zamtundu
uliwonse waanthu, ngakhale anamkungwi ndiena alindi udindo
owonetsetsakuti zimenezi sizikusokoneza chitukuko m’dziko.

No comments: