Tuesday, July 20, 2010

Njinga zangolo zingachepetse umphawi

WOLEMBA RICHARD CHIROMBO
Nduna yoona zaanthu okalamba ndiolumala, aReen Kachere, adati njinga
zomwe amayendera anthu olumala zingakhale njira imodzi yochepetsera
umphawi ngati anthuwo angamakoke ngolo, m’mene zimakhalira
ndiambulansi zanjinga, ndikumanyamulira katundu wamalonda
osiyanasiyana.
AKachere adati kwanthawi yaitali anthu olumala akhala akungogwiritsa
ntchito njiza zawo poyendera, osadziwa kuti njingazo zingathandize
pochepetsa umphawi ndikupangitsa kuti ambiri mwaanthu olumala omwe
amapemphapempha thandizo m’miseu adzidziimira paokha.
Ndunayi idalankhula izi sabata latha mumzinda waBlantyre itakumana
ndiakuluakulu abungwe lam’dziko laNetherlands lotchedwa
Transport4Transport, lomwe limathandiza maiko osiyanasiyana ndingolo
zomwe zimagwiritsidwa ntchito ngati ambulansi zanjinga, chinthu chomwe
chathandiza kuchepetsa infa zaamayi apakati m’maiko okwera kumene.
“Unduna wanga wakambirana ndiakuluakuluwa zokuti apereke thandizo
lazachuma komanso ngolo zomwe anthu olumala angamagwiritse ntchito
ponyamulira katundu wamalonda ngati njira imodzi yothetsera umphawi,”
adatero aKachere.
Iwo adati anthu okalamba, omwe kawirikawiri amakumananso ndimavuto
akayendedwe chifukwa chofooka m’thupi, angapindulenso ndingolozi
popeza kuti angamanyamule katundu wambiri ndiolemera mosavuta.
“Bungwe limeneli lakhala likuthandiza mabungwe ena dziko laMalawi
kuyambira chaka cha2007, koma lakhala likulimbikira pantchito
yochepetsa infa zaamayi apakati pomapereka ndalama zopangira ambulansi
zanjinga. Panopo tangolipempha kuti liyambenso kuthandiza olumala
ndiokalamba pomapereka ngolo zanjinga,” idatero ndunayi.
Nawo aRoel Barkhof, womwe ndiwapampando wabungwe
laTransport4Transport- lomwe silopanga phindu koma limapeza ndalama
zake kuchokera kukampani ina yam’dziko laNetherlands yotchedwa
Wagenborg- adati ali okonzeka kuyamba kuthandiza dziko laMalawi
ndingolo kuti olumala ndiokalamba adzinyamulira katundu.
“Ife takhala tikubwera ndikuthandiza mabungwe oposa atatu kuno
kuMalawi kuyambira m’chaka cha2007, ndipo tili okonzeka kuyamba
kuthandiza mwanjira iliyonse kuti miyoyo yaAmalawi itukuke.
Timagwiritsa ntchito ndalama zokwana K53, 000 pangolo iliyonse, ndipo
tathandiza kale kupanga ngolo zanjinga zaambulansi zokwana 400,”
adatero aBarkhof.
Iwo adati bungwe lawo lili lokonzeka kuyamba ntchitoyi nthawi
iliyonse, ndipo lidzagwira ntchito yopanga ngolozi kudzera kukampani
yotchedwa ‘Sakaramenta’, yomwe ndiyakuMalawi kom’kuno ndipo ili
kwaChemussa m’boma laBlantyre.
Mkulu waSakaramenta, aPeter Meijer, adati ali okonzeka kuyamba
ntchitoyi popeza kuti akhala akugwira kale ntchitoyi ndibungwe
lakuNetherlands’li kwazaka zoposa zitatu tsopano.
“Ife tili okonzeka kuyamba ntchitoyi. Tikufuna kuthandiza boma
laMalawi potukula miyoyo yaanthu ovutika. Chosangalatsa n’chakuti
kampani yathu idayambanso kale kuthandiza Amalawi popeza timalipilira
ogwira ntchito athu sukulu, chinthu chomwe chidasangalatsa anthu
akuNetherlands’wa ndikuapangitsa kumathandiza mabungwe m’dziko muno,”
adatero aMeijer.

No comments: