Friday, September 18, 2015

MATENDA A NG’OMBE A ZILONDA MMAPAZI NDI MKAMWA (FOOT AND MOUTH DISEASE) MBOMA LA CHIKHWAWA, KU SHIRE VALLEY ADD

Unduna wa Malimidwe, Ulimi Othirira ndi Chitukuko cha Madzi

CHIDZIWITSO




Unduna wa Malimidwe, Ulimi wa mthirira ndi chitukuko cha madzi ukudziwitsa anthu onse kuti kwagwa matenda a ng’ombe a zilonda m’ mapazi ndi m’mkamwa (omwe pa chizungu amatchedwa ‘Foot and Mouth’ )kudera la dipi ya Mthumba , Ku Mitole EPA, m’boma la Chikhwawa ku Shire Valley ADD.

Matenda a zilonda m’ mapazi ndi m’mkamwa a ng’ombewa ndi oopsya kwambiri chifukwa ndiopatsirana (Ziweto zokha-zokha) ndipo amagwira ziweto makamaka ng’ombe.  Ziweto zina zomwe zikhoza kukhuzidwa ndi monga mbuzi, nkhumba, nkhosa ndi ziweto za kutchire monga Njati.  Matendawa amabwezeretsa chitukuko mmbuyo ngati ziweto sizitetezedwa ndi kuthana ndi vutoli mwa msanga. Akuluakulu a mu Dipatimenti yoona za ziweto akuyesetsa kupeza njira zotetezera ziweto ndi kuthana ndi matendawa.

Mogwirizana ndi lamulo lokhudza katetezedwe ka matenda a ziweto omwe ali m’ndime 66.02 ya malamulo a dziko lino komanso ndondomeko ya m’bungwe loona za ziweto padziko lonse lapansi lotchedwa ‘World Animal Health Organisation’, Undunawu ukudziwitsa anthu onse kuti wayika njira zoyenera izi zothana ndi vutoli m’dera la Mthumba dipi thanki:

  • Kuletsa kugulitsa ziweto monga ngombe, mbuzi, nkhosa ndi nkhumba kwa kanthawi kochepa.
  • Kuletsa kupha  ziweto monga ngombe, mbuzi, nkhosa ndi nkhumba kwa kanthawi kochepa.
  • Kuletsa kuyenda ndi ziweto kapena zakudya za ziweto kuchokera kudera lokhudzidwali kupita ku madera ena.
  • Kuyimitsa kupereka ziphaso zovomerezeka kuyenda ndi ziweto.

Pomaliza Undunawu ukupempha anthu onse kuti agwirizane ndi ogwira ntchito ku Dipatiment yoona za ziweto ndi a Polisi potsatira njira zalembedwazi kuti matendawa asapitirire kufala.

Mukafuna kudziwa zambiri za mliriwu, lumikizanani ndi anthu awa: Dr B. Chimera, Dr P. Chikungwa ndi Dr G. Njunga pa manambala awa: 0999315766, 0888371509 ndi 0995910460.

signed

Erica Maganga (Mrs)

Mlembi Wamkulu mu Unduna wa Malimidwe, Ulimi Othirira ndi Chitukuko cha Madzi

17/09/2015

No comments: