Sunday, December 1, 2013
UTHENGA WAPADERA PA NKHANI YA KUBEDWA KWA CHUMA CHA BOMA
Mau oyambirira:
Ife, Aepiskopi a Mpingo Wakatolika muno M’malawi, takhala tikutsatira mokhumudwa nkhani imene yaululika yokhudza kubedwa kwa chuma chochuluka cha Boma, yomwe mwachidule ikutchulidwa kuti ‘Cash gate’. Tinaona kuti ndibwino kuti tikhale chete kwa nthawi yokwanira ndithu kuti timvetse zimene zinachitika, tilingalire ndiponso tipemphere pa zomwe zaululikazi. Ife tikanali odabwa kuona kuti zoterezi zingachitike m’dziko lathu lino limene anthu ake ngoopa Mulungu.
Nkhani yoipa ngati imeneyi njochititsa manyazi kwa dziko, ndipo ndi chizindikiro chosonyeza kulowa pansi kwa umunthu komanso kwa mtima wokonda dziko lathu kuno kwanthu. Tili okhumudwa kuona kuti mkhalidwe wokonda chuma, katangale ndinso nthenda yofuna kulemera mwamsanga zikukulirakulira pakati pathu; mmalo mwa mtima wokonda choona, wachilungamo ndi wogwira ntchito molimbika. Pakati pa zochitika zonsezi, ife abusa anu taona modzichepetsa komanso moona mtima, kuti tiyenera kusinkhasinkha pa za nkhani ya ‘Cash gate’ imeneyi, zotsatira zake zakubedwa kwa chuma chabomachi, ndiponso kuti tiperekeko maganizo pa zimene ziyenera kuchitika mofulumira.
Mfundo zake za nkhaniyi:
Mu nkhani yoipa imeneyi ife tikuonamo mfundo izi:
- Ndalama zambiri zimene zimayenera kugwira ntchito yothandiza anthu zabedwa chifukwa cha mtima wodzikonda mmalo moti chumacho chipindulire dziko pa ntchito yotukula miyoyo ya anthu.
- Panali ukathyali woopsa umene ena anakonza mogwirizana kuti abe chuma cha Boma, chinthu chimene chikuonetsa kuti khalidwe loyipa lazika mizu pakati pathu.
- Ndondomeko yoyendetsera ndi kulondoloza chuma cha Boma yafooketsedwa chifukwa cha kugwirizana kwa anthu osowa ungwiro.
Zotsatira za mchitidwe wakuba:
Ife tikuyamikira ntchito yomwe ikuchitika kale yofuna kupeza tsinde la mchitidwe woonangawu imene ikuchitika ndi Boma, mabungwe omwe si a Boma, magulu othandiza dziko la Malawi pa chitukuko ndiponso mtundu wonse wa Amalawi. Komabe, tikuona kuti ndibwino kuti titsindike zinthu izi:
- Umphawi utha kuonjezekera pakuti zinthu zitha kupitirira kukwera mtengo chifukwa cha kusowa kwa mfundo zothandiza zokomera anthu komanso kubedwa kwa chuma cha Boma;
- Thandizo la chuma lopita ku Boma lochokera ku maiko amene amathandiza dziko lathu lino likayimitsidwa, ndiye kuti ndalama yathu igwa mphamvu kwambiri, chinthu chimene chidzabweretsa mavuto aakulu a zachuma pakuti mitengo ya katundu ndi ntchito zina zidzakwera;
- Vuto la kusowa kwa ndalama zakunja limene libwere chifukwa chakuti maikowa asiya kuthandiza Boma kudzachititsa kuti dziko lino livutike kwambiri kuti likwanitse kulipira zinthu zimene zimachokera kunja monga mankhwala ndi zipangizo zaulimi, makamaka panyengo ino pamene chuma cholowa m’dziko lino chimakhala chochepa;
- Amalawi eni ake ndiponso iwo amene amakhoma misonkho avutika mnjira zambiri; poyamba, iwo aberedwa kale chuma chawo m’njira zachinyengo; kachiwiri, anthu ake omwewo okhoma misonkhowo saona chitukuko chimene chikadachitika m’dera lawo chifukwa cha kuchepetsedwa kwa ndalama zochokera ku Boma ku ntchito zake; ndipo potsiriza, ndi anthu omwewo amene adzalipire milandu yonse yokhudza kubaku, popeza kuti ntchito yonseyo itheke, Boma lidzasowa kugwiritsa ntchito ndalama za misonkho yawo yomweyo.
Zoyenera kuchita:
Titalingalira zonsezi, ife tikupempha kuti zotsatirazi zichitike:
Boma:
Pakhazikitsidwe ndondomeko yooneka ndiponso yodalirika imene ingathandize kulimbikitsa chikhulupiriro cha anthu mwa Boma, kupanda apo anthuwa adzapitirira kuponderezedwa ndiponso kulipira ndalama pamene ena aba:
- Pachitike kafukufuku mofulumira monga akusowekera pakadali pano; Boma lichite ntchito imene likuyenera kuchita kuti anthu ayambenso kulikhulupirira.
- Maofisala a Boma pamodzi ndi onse okhudzidwa avomere modzichepetsa gawo lawo pa kubedwa kwa chuma kumeneku.
- Koposa kungomanga anthu, pakhazikitsidwe ndondomeko yooneka bwino, yobwezeretsera chuma chaboma chimene chabedwachi, pakuti izi zidzathandiza kuti anthu aone kuti pali chilungamo. Pakutero, chuma chimene chinabedwachi chidzabwereranso kwa Amalawi popeza ndiwo amene akuvutika chifukwa cha ‘Cash gate’.
- Boma likhale lokonzeka kumvetsera moona mtima maganizo a anthu amene akulira ndipo ataya mtima chifukwa cha vuto limeneyi.
Magulu othandiza pa chitukuko cha dziko:
Maiko ndi mabungwe amene amapereka chithandizo ku bajeti ya Boma apeze njira zina mwamsanga zothandizira Amalawi pamene Boma likuyesetsabe kukonzetsa dongosolo lake loyendetsera chuma. Amalawi osalakwa asavutike chifukwa chakuti maiko ndi mabungwewo aimitsa kapena kuchedwetsa thandizo lao.
Amalawi:
- Amalawi onse akuyenera kukhala pansi, kudzifunsa, ndi kutembenuka mtima, pokumbukira kuti ngakhale tiyenera kuyankha kwa nzika za dziko lino, koposa tiyenera kupereka yankho kwa Mulungu pa katundu wa dziko.
- Anthu onse amene akukhudzidwa ndi mchitidwewu asiyiretu, pakuti izi zikukutsana ndi Malamulo a Mulungu; ndipo zikutilepheretsa kuona chitukuko ndi kulemekezana monga mmene zimayenera kukhalira pakati pa ana a Mulungu.
- Pakuti ndondomeko zosamalira chuma zimakhala m’manja mwa anthu amene ayenera kukhala angwiro, iwo amene akuyendetsa ndi kusamalira ndondomeko ya chuma cha boma ayenera kukhala okhulupirika, osamalira chuma cha ena ngati ana a Mulungu.
- Tikupempha ansembe ndi atumiki onse a mu Mpingo wa Katolika kuti asagwiritse ntchito vuto la kubedwa kwa ndalama m’boma - ‘Cash gate’ - ngati mwayi woti alimbikitsire kusiyana maganizo pakati pa zipani zandale. M’malo mwake, iwo akumbukire pempho lathu lomwe takhala tikunena mobwerezabwereza kuti cholinga cha Mpingo wa Katolika sikuchitira anthu chisankho pa maganizo a ndale.
Mau otsiriza:
Nkhani ya ‘Cash gate’ yatikhudza kwambiri tonsefe. Tikubwereza kudzudzula mchitidwe woyipawu ndiponso tikufuna kuonetsa umodzi wathu ndi onse amene akuchitapo kanthu, kuti dziko lathu la Malawi lisapitirire kutaya mwayi wa chitukuko.
Vuto limene lagwera dziko lathu lino silingathetsedwe pochita ndale kapena pongokambirana chabe ngati anthu, ayi; kwa ife, vuto limene Malawi wakomana naloli likukhudza moyo wauzimu. “Mdani amene tiyenera kulimbana naye kuti tipeze ufulu weniweni ndi tchimo komanso ndondomeko zolakwika zimene tchimolo limadzetsa pamene likunka likulirakulira ndi kufalikira. ” Tchimo la munthu aliyense payekha ndiponso tchimo lopezeka pakati pathu ndi lokhudza ndondomeko zoyendetsera dziko, zimalimbikitsana. “Pakutero, tchimo limanka likulirakulira, kufalika, ndi kukhala gwero la machimo ena, mpaka kusokoneza chikhalidwe cha anthu.”
Pokhala Fuko loopa Mulungu, tikupempha Amalawi onse kuti atembenuke mtima ndi kuyamba kukometsa chikhalidwe chao.
Right Reverend Joseph M. Zuza Chairman and Bishop of Mzuzu,
Most Reverend Thomas Msusa Vice Chairman, Bishop of Zomba and Archbishop designate of Blantyre,
Most Reverend Tarsizio G. Ziyaye Archbishop of Lilongwe,
Right Reverend Peter Musikuwa Bishop of Chikwawa,
Right Reverend Emmanuel Kanyama Bishop of Dedza,
Right Reverend Alessandro Pagani Bishop of Mangochi,
Right Reverend Martin Mtumbuka Bishop of Karonga,
Right Reverend Montfort Stima Diocesan Administrator and Auxiliary Bishop of Blantyre.
Dated: First Sunday of Advent, 1 December, 2013.
Subscribe to:
Post Comments (Atom)
No comments:
Post a Comment