Friday, August 14, 2015

Kulengeza Uthenga Wachisoni

14 August, 2015

Kulengeza Uthenga Wachisoni

A ku likulu la Mpingo Wakatolika akulengeza za imfa ya Bambo Denis Kamalo a Zomba Dayosizi. Bambo Kamalo amwalira ku chipatala cha Mission cha Pirimiti m’boma lomwelo la Zomba dzulo pa 13 August ali ndi zaka 74.

Mwambo wa Maliro ukachitikira ku Zomba Cathedral Lolemba pa 17 August, 2015 kuyambira 10:00 mmawa.

Bambo Kamalo omwe anabadwa pa 14 September, 1941, amachokera m’mudzi wa Kamaru ku Mlombozi Parish m’Boma la Zomba. Atatsiriza maphunziro awo a Philosophy and Theology adadzozedwa unsembe pa 18 April m’chaka cha 1971.

Moyo wa Unsembe:
Ngati wansembe, Bambo Kamalo atumikira ku Parishi ndi malo awa: Liwonde, Nankhunda, Lisanjala, Mayaka, Chipini, Domasi ndiponso Matiya. Adakhalapo Director wa Likulezi Catechetical Centre komanso St. Joseph Carpentry.

Bambowa adatumikiranso ngati Khansala wa Episkopi, Chaplain wa Achinyamata komanso Chaplain woyang’anira ndende ndi zipatala.

Dongosolo la mwambo wa maliro:
14 – 16 August, 2015: Thupi la malemuwa likhala likusungidwa kunyumba ya chisoni ya Chipatala chachikulu cha Zomba. Mapemphero akhala akuchitika opempherera mzimu wawo.

16 August, 2015:  4:00 madzulo:  Mapemphero ndi kutenga thupi la malemuwa kunyumba yachisoni.
  4:30 madzulo:  Mwambo wa Misa ku Zomba Cathedral.
  6:00 madzulo:  Mwambo wokhudza maliro.

17 August, 2015: 10:00 mmawa: Nsembe ya Misa ku Zomba Cathedral.


Mzimu wa Bambo Kamalo uuse ndi mtendere


Rev. Fr. Henry Saindi
SECRETARY GENERAL

No comments: