Saturday, February 14, 2015

UTHENGA WA PAPA FRANCIS WA PA TSIKU LOKUMBUKIRA ODWALA PA DZIKO LONSE LAPANSI 11 FEBRUARY 2015.

UTHENGA WA PAPA FRANCIS WA PA TSIKU LOKUMBUKIRA ODWALA PA DZIKO LONSE LAPANSI 11 FEBRUARY 2015.

“Ndinali ngati maso kwa anthu osapenya
Ndinali ngati mapazi kwa anthu opunduka”
(Yobu 29:15)

Abale mwa Khristu,

Pa tsiku ili la 11 February 2015 lokumbukira ndi kuganizira odwala pa dziko lonse lapansi, lidakhazikitsidwa ndi Papa Yohane Paulo Wachiwiri Woyera, ndikuyang’ana kwa inu nonse olemedwa ndi matenda ndipo muli olumikizidwa mwa njira zosiyanasiyana ku thupi la Yesu Khristu ozunzidwa. Komanso ndikuyang’ana kwa inu nonse madokotala ndi anthu ena onse ogwira ntchito zaumoyo modzipereka chabe.

Mfundo ya chaka chino ikutipempha kuti tisinkhesinkhe pa mau a m’Buku la Yobu onena kuti, “Ndinali ngati maso kwa anthu osapenya, ndinali ngati mapazi kwa anthu opunduka” (Yobu29:15). Ndidakakonda kusinkhasinkha mau amenewa potsamira pa mau awa “sapientia cordis” kutanthauza nzeru zamumtima.

  1. “Nzeru izi” simaganizo chabe kapena chinthu chosaoneka chochokera m’mutu chabe. Koma ndi chinthu chomwe monga adanenera Yakobe Woyera m’kalata yake, “Koma nzeru zochokera kumwamba, poyamba nzangwiro, kuwonjezera apo nzamtendere, zofatsa ndi zomvera bwino. Ndi zachifundo chambiri, ndipo zipatso zake zabwino nzochuluka. Nzeruzo sizikondera kapena kuchita chiphamaso.” (Yakobe 3:17). Ndi njira yoonera zinthu zoikidwa ndi Mzimu Woyera m’maganizo ndi m’mitima ya amene amakhudzidwa ndi mavuto a abale ndi alongo ao ndiponso amene angaone mwa abalewo chithunzi cha Mulungu. Pa chifukwa ichi, tiyeni titenge pemphero la mlakatuli wa Masalimo; “Tsono tiphunzitseni kuwerenga masiku athu, kuti tikhale ndi mtima wanzeru.” (Salimo 90:12). “Nzeru izi zamumtima,” zomwe ndi mphatso yochokera kwa Mulungu ndi zipatso za Tsiku Lokumbukira ndi Kuganizira Odwala.

  1. Kukhala ndi nzeru zamumtima kutanthauza kutumikira abale ndi alongo athu. Mau a Yobu oti, “Ndinali ngati maso kwa osapenya, ndinali ngati mapazi kwa opunduka,” akunena za munthu wolungama amene adasangalala chifukwa cha udindo kapena mphamvu zaulamuliro umene anali nawo pakati pa akuluakulu amumzinda umene umaperekedwa kwa amene anali osowa. Chimwemwe chake chinali kutsamira pakupereka thandizo kwa osauka amene ankasowa thandizo lake ndiponso pakusamalira ana ndi akazi amasiye (Yobu 29:12-13).
Masiku ano, ndi Akhristu angati amene amaonetsa, osati ndi mau ao chabe, koma ndi moyo ndiponso ndi ntchito zao zotsamira pa chikhulupiriro, kuti iwo ndi “Maso kwa osapenya” ndiponso “Mapazi kwa opunduka?” Iwo amakhala pafupi ndi odwala amene amasowa chisamaliro pafupipafupi ndipo amasowa thandizo loti nkuwachapira, kuwaveka ndiponso kuwadyetsa. Utumiki umenewu, makamaka pamene ukhala wotenga nthawi yaitali umatopetsa ndi kulemetsa. Ndi chapafupi kuthandiza munthu masiku ochepa, koma chimakhala chovuta kusamalira wodwala kwa miyezi kapena kwa zaka zingapo, ndipo chimakhala chokhumudwitsa pa zomwe akuchita. Komatu njira iyi ndi yopambana chifukwa imachititsa munthu kukhala woyera. Mu nthawi ya masautso ndi imene mwapadera, tiyenera kukhala pafupi ndi kudalira Ambuye Yesu, potero, timathandizira pa utumiki wa Mpingo.

  1. Nzeru zamumtima zitanthauza kukhala limodzi ndi abale ndi alongo athu. Nthawi yokhala ndi odwala ndi nthawi yoyera. Ndi njira yotamandira Mulungu amene amatichititsa kuti tikhale ndi nkhope/chithunzi cha Mwana wake, amene “adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka. Yesu yemwe adati, “Koma Ine ndili pakati panu ngati wotumikira.” (Luka 22:27).

Ndi chikhulupiriro cholimba tiyeni tipemphe Mzimu Woyera kuti atipatse chaulere chotithandiza kuti tizipeza nthawi yokhala pafupi ndi abale ndi alongo odwala. Kukhala nawo pafupi chifukwa chokhudzidwa ndi matenda awo, odwala amalandira chikondi ndipo amathuzitsidwa mtima. Ku mbali inayi zimakhala zodabwitsa kuti anthu ena amalankhula za kufunika kokhala ndi “Moyo wabwino” ngati kuti kukhala ndi moyo wodwaladwala kwambiri sichinthu chomuyenera munthu.

  1. Nzeru zamumtima zitanthauza kudzipereka ndi kudziiwala pofuna kutumikira abale ndi alongo athu odwala. Nthawi zina dziko lapansi limaiwala kufunikira kokhala pafupi ndi bedi la wodwala chifukwa timaoneka kuti tili ofulumira nthawi zonse, pamene tikutanganidwa ndi zathu zokha nkumaiwala zoti nthawi zina tizipeza nthawi yokhala pafupi ndi odwala nkumawathuzitsa mtima. Mchitidwe osalabadira odwala umalimbikitsidwa ndi chikhulupiriro chochepa chomwe chimatiiwalitsa mau a Ambuye athu Yesu Khristu oti, “Munkachitira Ine amene” (Mateo 25:40).

Chifukwa cha ichi, ndikubwerezanso kutsindika pa mfundo yakuti pa zonse, “Tizitsogoza mtima wakudziiwala ndi wodzipereka chifukwa chofuna kutumikira abale ndi alongo athu odwala ngati njira yokwaniritsa lamulo lalikulu lachikondi ndiponso ngati njira ya moyo wathu wauzimu pothokoza chifukwa cha mphatso yaulere imene Mulungu adatipatsa. (Evangelii Gandium, 179). Utumiki wa Mpingo ndiye kasupe wa mtima wopereka mwaulere ndiponso wa mtima womvetsa, wothandiza ndi kupititsa patsogolo ntchito zachifundo”.  1. Nzeru zamumtima zitanthauza kukhala ndi mtima wokhala amodzi ndi anzathu odwala kwinaku tisakuwaweruza. Chifundo chimatenga nthawi yaitali. Monga adachitira abwenzi a Yobu: Adakhala ndi Yobuyo masiku asanu ndi awiri, usana ndi usiku womwe. Koma panalibe ndi mmodzi yemwe amene ankalankhula naye. Chifukwa chozindikira kuti Yobuyo akuvutika kwambiri. Ngakhale zinali choncho, abwenzi a Yobuyo anali kumuweruza m’mitima mwao: ankaganiza kuti mazunzo a Yobu anali chilango chochokera kwa Mulungu chifukwa cha machimo ake. Chikondi ndiponso chifundo chenicheni ndi chimene chimalola kugawana popanda kuweruza kapena chiphamaso. Chikondi chotere chimangoyamika ndi kukhutira pa zabwinozo.

Kuzunzika kwa Yobu kumapeza mayankho enieni pa mtanda wa Yesu, amene ali chizindikiro chakuti Mulungu ali nafe, mwaufulu ndi mwachifundo chodzaza. Chikondi chotere chokonda munthu wozunzika, makamaka kwa amene amazunzika popanda zifukwa, chimakhala pa thupi la Yesu wouka kwa akufa mpaka muyaya; zilonda zake zaulemerero ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro (Malaliko a Papa Francis pa otchula Yohane wa XXIII ndi Yohane Paulo WAchiwiri kuti ndi Oyera, pa 27 April, 2014)

Ngakhale kuti matenda kapena zinthu zina zokhoma zimatilepheretsa kufikira abale athu, kuzunzika kungathe kukhala mwai wopereka zaulere ndiponso kungathe kusanduka kasupe wa kupeza ndi kukula m’nzeru. Timafika pomvetsa momwe Yobu, kumapeto kwa moyo wake adanena kuti, “Ndinkangomva za inu ndi makutu koma tsopano ndakuwonani chamaso.” (Yobu 42:5). Anthu amene ali m’mavuto ndi mu ululu, akavomereza mazunzo ao ndi chikhulupiriro, angathe kusanduka mboni zenizeni za chikhulupiriro chotha kulandira mazunzo, ngakhale asamvetse tanthauzo lake.

  1. Ndikupereka tsiku ili Lokumbukira ndi Kuganizira Odwala pa dziko lonse lapansi m’chitetezo cha Amai Maria, amene adatenga pathupi ndi kubereka Nzeru: Yesu Khristu, Ambuye athu.

O! Amai Maria, Mpando wa Nzeru, pemphererani, ngati Mai wathu, odwala onse ndi onse amene akuwasamalira, kudzera mu utumiki wathu kwa abale athu odwala, ndipo kuti kudzera m’kudwala tithe kulandira ndi kukhala ndi mtima wanzeru!

Ndi pemphero ili lopempherera inu nonse, ndikukupatsani Madalitso Aupostoli wanga.

Kuchokera ku Vatikani, 3 December, 2014.

Tsiku lokumbukira Francis Xavier Woyera.

FRANCIS

No comments: